A Putaputa anena izi kutsatila zomwe wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa boma la Likoma a Charles Chilambula anabweza zina mwazitukuko zomwe anthu am’bomali adasankha kudzera kuma Village Development Committee VDC.
“tikulankhulana ndi akukhonsolo cholinga chakuti tiphunzire bwino kenako tikasanthure zitukuko zomwe zichitike pazaka zisanu zikudzazi”, atero a Putaputa.
Masiku apitawa a Chilambula anayitanitsa akomiti oyang’anira zitukuko zakudera kuwakumbutsa kuti pakali pano ndalama ya CDF ndiyochuluka kusiyana ndizaka zam’mbuyomu choncho anthu akudera akuyenera kusankha zitukuko zolingana ndi ndalamayi.
“ena anapempha zigayo ena zimbudzi zam’mbali mwanyanja zomwe asodzi angakwanitse pawokha titayika malamulo apadera”, anatero a Chilambula.
Iwo analangiza nyumbayi kuti 5 billion ikufunika zitukuko zikuluzikulu monga misewu yabwino, kuyika zofunikira mzipatala, kukonza malo otsikira ndi kukwera sitima pa chilumba cha Chizumulu komanso kukonza sukulu za sekondale.
Koma titalankhula ndi mlangizi wa zachitukuko m’bomali a Uledi Mpeta atiuza kuti makomitiwa aphunzitsidwa sabata ino ndithandizo la ndalama zomwe phungu wa Likoma wapeleka koma ati maphunzilowa achitika tsiku limodzi ngakhale amafunika kuti achitike kwa masiku atatu kaamba kakusowa kwa ndalama.