Khonsolo ya Likoma yati mwayi wa ntchito zosiyanasiyana ulipo mukhonsoloyi kwa achinyamata omwe ali ndi zowayeneleza.

Poyankha funso la phungu wa Likoma a Christopher Ashems Songwe lomwe anafunsa lachisanu pa mkumano wa Full Council lokhudza ndondomeko zakalembedwe ka ntchito pakhonsoloyi, a Banabas Sambamo omwe ndi wapampando wa khonsoloyi anati ndizosavuta kulemba ntchito achinyamata ochokera m’bomali chofunika ndikukhala ndizowayeneleza.

A Sambamo anapitiliza kunena kuti posachedwapa akhala akutulutsa chikalata cha mwayi wantchito za Umoyo komanso magawo ena ndipo panthawiyi alankhulana ndi bwana mkubwa wa Likoma kuti achinyamata aku Likoma adzakhale ndi mwayi olembedwa ntchito.

Wayimilira achinyamata ku khonsoloyi Macfallen Mafuta wati ndizoona kuti achinyamata ambiri amakhala kuti zowayeneleza alibe kotero iye wati apita kumakalabu kukalimbikitsana ndi anzake za nkhaniyi.

Likomafm, Onlinenews.

Related posts

‎kutsatila kutsegulira kwa sukulu pa 22 September chaka chino, gulu la achinyamata lochokera kwa a mfumu a Mani m’mudzi wa Mbungo lapeleka makope ndi zolembera kwa ana apasukulu ya mbungo m’boma la Likoma.‎‎

Mulandu wayemwe akumuganizira kuti ndi m’modzi mwawoyendetsa Boat lomwe linachita ngozi ndikupha anthu nkhumi ndi modzi m’mawa wapa 12 April, 2025, m’boma la Likoma wayamba lero.

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo yati mitambo ya mvula ya mabingu yayambapo kale kusonkhana m’madera ena am’dziko muno.