Malingana ndi oyimira boma pa milandu Sub-Inspector Shallnever Mfune adauza khothili kuti usiku wapa 25 July 2026 odandaulayu adatseka nyumba yake koma m’mawa wake anapeza sutikesi ya mdzukulu wake itasowa.
“Sutikesi ndi zinthu zomwe zinali mkati mwake zinali zandalama zokwana 2 million kwacha ndipo zina mwa zinthuzi ndi nsapato, mashati, jazi, mathalauza, yunifolomu za kusukulu, mabulangete komanso 50 sauzande kwacha mwazina”.
First grade magistrate Fordwatch Nyamazana Mkandawire wati wapeleka chilangochi kaamba koti mlandu wakuba katundu wa ophunzira ndi waikulu chifukwa choti umasokoneza maphunziro.
Kingsley Lamwele, amachokera m’mudzi wa Zambala mfumu yaikulu Mwadzama m’boma la Salima.