Mulandu wayemwe akumuganizira kuti ndi m’modzi mwawoyendetsa Boat lomwe linachita ngozi ndikupha anthu nkhumi ndi modzi m’mawa wapa 12 April, 2025, m’boma la Likoma wayamba lero.

Malingana ndi His Worship Fordwatch Nyamazana Mkandawire wati mlanduwu ukuyembekezeka kupitilira lachisanu sabata ino.

Naye otengera milandu ku bwalo lamilandu Sergeant Charles Chilala wati lachisanu abweletsa mboni zawo zonse ndicholinga choti oganizilidwayu asachedwe kuweluzidwa.

Woganizilidwayu ndi a Owen Gondwe ochokera m’boma la Rumphi adzaka 22.

LikomaFM, OnlineNews

Related posts

‎kutsatila kutsegulira kwa sukulu pa 22 September chaka chino, gulu la achinyamata lochokera kwa a mfumu a Mani m’mudzi wa Mbungo lapeleka makope ndi zolembera kwa ana apasukulu ya mbungo m’boma la Likoma.‎‎

Khonsolo ya Likoma yati mwayi wa ntchito zosiyanasiyana ulipo mukhonsoloyi kwa achinyamata omwe ali ndi zowayeneleza.

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo yati mitambo ya mvula ya mabingu yayambapo kale kusonkhana m’madera ena am’dziko muno.