Opindula ndi ndondomeko ya mtukula pakhomo m’boma la Likoma ati njira yatsopano yolandila ndalama kudzera pa phone ndiyodalilika.

SCT Program Coordinator

Izi zadziwika Likoma radio itayendera ena mwa opindula ndi ndondomekoyi pa chilumba cha Chizumulu kufuna kunva momwe opindulawa ayilandilila njila yamakonoyi yomwe pachingelezi akuti E Payment.

Mayi Ayida Dewa am’mudzi wa Chiunda pachilumbachi ati pomwe ankalandila thandizoli pamanja amatha kutenga tsiku lonse akudikila kuti alandile ndalama zawo komanso aliyense amadziwa kuti ali ndi ndalama, “njira yamakonoyi ndiyachisisi komanso ndimatenga ndalama nthawi yomwe ndafuna”.

Nawo a Herbet Kakusa ati palibe vuto lililonse lomwe akumana nalo ndinjila yamakonoyi ndipo sataya nthawi pokatenga ndalamayi kwa ajenti.

Pothilapo ndemanga mkulu oyang’anila pologalamu ya mtukula pakhomo boma la Likoma a Christopher Kanaza ati pomwe ankapeleka ndalamazi pamanja zimawatengera masiku awili kupeleka ndalamazi koma njilayi yapeputsa ntchito yawo, ndipo apempha omwe amalandila ndilamazi kugwilitsa ntchito moyenela kuti mabanja awo atukuke.

Mtukula pakhomo ndi ndondomeko ya boma yomwe inakhazikitsidwa kuti idzipereka thandizo la ndalama ku mabanja ovitikitsitsa omwe alibe kuthekera kogwila ntchito ndicholinga chochepetsa umphawi.

Related posts

‎kutsatila kutsegulira kwa sukulu pa 22 September chaka chino, gulu la achinyamata lochokera kwa a mfumu a Mani m’mudzi wa Mbungo lapeleka makope ndi zolembera kwa ana apasukulu ya mbungo m’boma la Likoma.‎‎

Mulandu wayemwe akumuganizira kuti ndi m’modzi mwawoyendetsa Boat lomwe linachita ngozi ndikupha anthu nkhumi ndi modzi m’mawa wapa 12 April, 2025, m’boma la Likoma wayamba lero.

Khonsolo ya Likoma yati mwayi wa ntchito zosiyanasiyana ulipo mukhonsoloyi kwa achinyamata omwe ali ndi zowayeneleza.