Pofuna kupititsa patsogolo maphunziro mdziko muno wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo ndi ukhondo yemwenso ndi phungu wa pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu wolemekezeka a Charles Chilambula apereka mabuku ku ofesi yoona za maphunziro m’boma la Likoma.

Mabukuwa ndi thandizo lochokera ku Malawi National Library Services ngati mayankho pazokambilana zimene mbali ziwirizi zinachita.

Iwo awuza adindo kuti kubwera kwa mabukuwa kuthandiza kulimbikitsa ophunzira chikhalidwe chowerenga.

“Titapempha kuti sukulu zathu zili ndi nyumba zowelengelamo zomwe mulibe mabuku atithandiza ndi mabuku oposa 4,000, omwe athandizire ana athu kukonzekera kokwanira”.

A Chilambula ati atengapo mbali kuti mabukuwa afike m’boma la Likoma polipilira mayendedwe ndi ogwira ntchito kuti mabukuwa afike ku Likoma.

Polandira mabukuwa bwana mkubwa wa boma la Likoma Abubakar Nkhoma ayamikira phunguyu kaamba ka thandizoli ndipo ati mabukuwa afikira sukulu zonse za pulayimale ndi sekondale m’bomali.

Boma la Likoma lili ndi sukulu khumi za pulayimale komanso ma sekondale atatu aboma.

LikomaFM,OnlineNews.

Related posts

Khothi la first grade magistrate ku Likoma lagamula a Kingsley Lamwele a zaka 18 kukakhala kundende ndikukagwila ntchito yakalavula gaga kwa zaka zinayi kaamba kolowa m’nyumba ndi kuba katundu osiyanasiyana.

Apolisi m’boma la Likoma amanga a Charlse Banda, powaganizira kuti anachita chipongwe msungwana wazaka khumi.

Wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo yemwenso ndi phungu wa Likoma Islands Constituency a Charles Chilambula ati kubwera kwa incinerator m’boma la Likoma kupititsa patsogolo ntchito za umoyo.