‎kutsatila kutsegulira kwa sukulu pa 22 September chaka chino, gulu la achinyamata lochokera kwa a mfumu a Mani m’mudzi wa Mbungo lapeleka makope ndi zolembera kwa ana apasukulu ya mbungo m’boma la Likoma.‎‎

M,modzi mwa achinyamata omwe apelereka makopewa a Nick Mkuyamba ati cholinga chachikulu cha gulu lawo ndikupititsa patsogolo maphunziro musukulu za primary m’bomali.‎‎Nawo a Gresham omweso ndi m’modzi mwa achinyamatawa ati achinyamata ali ndi udindo othandiza pachitukuko chadziko munjira zosiyanasiyana.

“makolo ena kapezedwe kawo ndikovutikila ndichifukwa tinaganiza kuti pomwe sukulu zatsegulira titengepo mbali”.

‎M’modzi mwa ana opindula Monica Gama wathokoza achinyamatawa ndipo wati thandizoli limuthandizira kuti maphunziro ake ayende bwino.

‎Achinyamatawa apeleka makope asanu ndi limodzi ndi zolembera ziwiri kwa ana okwana 34.

LikomaFM, OnlineNews.

Related posts

Mulandu wayemwe akumuganizira kuti ndi m’modzi mwawoyendetsa Boat lomwe linachita ngozi ndikupha anthu nkhumi ndi modzi m’mawa wapa 12 April, 2025, m’boma la Likoma wayamba lero.

Khonsolo ya Likoma yati mwayi wa ntchito zosiyanasiyana ulipo mukhonsoloyi kwa achinyamata omwe ali ndi zowayeneleza.

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo yati mitambo ya mvula ya mabingu yayambapo kale kusonkhana m’madera ena am’dziko muno.