A Chilambula amalankhula izi lero pamwambo otsegulira chipatala chaching’ono cha YoMa chomwe chamangidwa m’mudzi wa Yofu m’boma la Likoma.
A Chilambula ati chipatalachi chichepetsa imfa ya ana ang’onoang’ono ndi amayi oyembekezera omwe amafuna thandizo lamsanga komanso chithandizila kuchepetsa matenda.
Polankhulapo wamkulu oyang’anila ntchito za umoyo m’bomali Dr Gracewell Mathewe ati kubwera kwa chipatalachi kusintha zambiri pankhani ya zaumoyo.
“Kutengera ndi level yachipatalachi tidzipereka uphungu kwa amayi oyembekezera, kupereka katemera kwa ana, komanso kuthandiza ngati munthu wavulala mwazina”, atero Dr Mathewe.
Nawo mayi Eneless John ochokera m’mudzi wa mfumu Mnyanje omwe ndiwombekezera pakadali pano ati chipatalachi chichepetsa mtunda omwe amayi oyembekezera amakumana nawo akamapita ku sikelo.
Chipatala cha YoMa chamangidwa ndi ndalama zakwana 146 million kwacha ya thumba la Constituency Development Fund, CDF.