Sitima ya MV Chilembwe idziyenda kawiri patsiku kuyambila pa 15 April pakati pa boma la Likoma ndi Nkhata Bay.

“Ndiyankha pompano zokhudza MV Chilembwe zomwe phungu wanyumba ya malamulo wapempha”, nduna yowona za mayendedwe ndi mtengatenga a Jacob Hara ndiwo anena izi pamwambo wotonthoza mabanja omwe akhudzidwa ndi ngozi yabwato yomwe yachitika pa 12 April m’boma la Likoma.

Ndunayi yalamula izi kutsatira pempho la phungu wadelari a Christopher Ashems Songwe.

Related posts

‎kutsatila kutsegulira kwa sukulu pa 22 September chaka chino, gulu la achinyamata lochokera kwa a mfumu a Mani m’mudzi wa Mbungo lapeleka makope ndi zolembera kwa ana apasukulu ya mbungo m’boma la Likoma.‎‎

Mulandu wayemwe akumuganizira kuti ndi m’modzi mwawoyendetsa Boat lomwe linachita ngozi ndikupha anthu nkhumi ndi modzi m’mawa wapa 12 April, 2025, m’boma la Likoma wayamba lero.

Khonsolo ya Likoma yati mwayi wa ntchito zosiyanasiyana ulipo mukhonsoloyi kwa achinyamata omwe ali ndi zowayeneleza.